Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.
Genesis 45:2 - Buku Lopatulika Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adalira momveka kotero kuti Aejipito adamva ndithu, ndipo mbiri ya zimenezo idakafika mpaka kwa mfumu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo analira mokweza mwakuti Aigupto anamva. Onse a ku nyumba kwa Farao anamvanso za zimenezi. |
Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.
Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo.
Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake.
Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.
Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.