Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Yosefe adauza abale ake kuti, “Ine ndine Yosefe. Kodi bambo wanga akali moyo?” Koma abale akewo adadzazidwa ndi mantha, kotero kuti sadathenso nkumuyankha komwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndine Yosefe! Kodi abambo anga akanali ndi moyo?” Koma abale ake sanathe kumuyankha chifukwa anali ndi mantha kwambiri pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:3
14 Mawu Ofanana  

Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chilombo; ndipo tidzaona momwe adzachita maloto ake.


Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.


Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanene kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa.


Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo?


Chifukwa chake ndiopsedwa pankhope pake; ndikalingirira, ndichita mantha ndi Iye.


Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka; chikukhudza, ndipo uvutika.


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope.


Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.


Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe anazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.


Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;


Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa