Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Tsono Yosefe adapita payekha kukalira misozi. Kenaka adabwerako nayambanso kulankhula nawo. Adapatulapo Simeoni, nammanga pomwepo iwowo akuwona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Yosefe anapita pambali payekha kukalira. Kenaka anabweranso nadzayankhula nawo. Iye anatenga Simeoni namumanga iwo akuona.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:24
15 Mawu Ofanana  

Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana aamuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m'mzinda napha amuna onse.


Ndipo sanadziwe kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira.


Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.


Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni.


Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo.


Ndipo Yosefe sanakhoze kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Tulutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ake.


Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao.


M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.


Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,


Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.


Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa