Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:1 - Buku Lopatulika

1 Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pamenepo mpingo wonse udafuula kwambiri, ndipo anthu adalira usiku umenewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Usiku umenewo gulu lonse la Aisraeli linalira mofuwula kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:1
13 Mawu Ofanana  

koma anadandaula m'mahema mwao, osamvera mau a Yehova.


Chingakhale ichi chonse anachimwanso, osavomereza zodabwitsa zake.


Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.


Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake.


Wa fuko la Asere, Seturi mwana wa Mikaele.


Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.


Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!


Koma simunafune kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu.


Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvere mau anu, kapena kukutcherani khutu.


Ndipo pamene Yehova anakutumizani kuchokera ku Kadesi-Baranea, ndi kuti Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ake.


Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.


Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa