Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 13:33 - Buku Lopatulika

33 Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Tidaonanso ziphona, (zidzukulu za Aanaki). Ifeyo tinkaoneka ngati ziwala, ndipo iwonso ankatiwona ngati ziwala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 13:33
17 Mawu Ofanana  

Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.


Anaphanso Mwejipito munthu wamkulu, msinkhu wake mikono isanu, ndi m'dzanja la Mwejipito munali mkondo ngati mtanda woombera nsalu; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wake womwe.


Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;


Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)


Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi mizindayo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki.


Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.


Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.


(Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki.


(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).


anthu aakulu ndi ataliatali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?


Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwachotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israele; Yoswa anawaononga konse, ndi mizinda yao yomwe.


Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi mizinda yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.


Ndipo Kalebe anaingitsako ana aamuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.


Ndipo Aisraele onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri.


Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa