Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:30 - Buku Lopatulika

30 Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Atanena zimenezo Yosefe adachokapo mofulumira chifukwa choti mtima wake udaadzaza ndi chifundo chifukwa cha mng'ono wake uja. Anali pafupifupi kulira, motero adapita m'chipinda mwake nakalirira m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Kenaka Yosefe anafulumira kutuluka chifukwa mtima wake unadzaza ndi chifundo cha mngʼono wake ndipo anafuna kulira. Tsono anakalowa mʼchipinda chakechake nakalira kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:30
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.


Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao.


Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake.


Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wake analankhula ndi mfumu, popeza mtima wake unalira mwana wake, nati, Ha? Mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani.


Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;


Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleke usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.


Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona,


Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.


Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,


Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;


pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndidzazidwe nacho chimwemwe;


Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa