Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.
Genesis 42:9 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakumbukira maloto aja onena za iwo, ndipo adati, “Ndinu anthu ozonda dziko. Mwabwera kuno kudzazonda kuti muwone ngati dziko lathu ndi lofooka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anakumbukira maloto aja amene analota za iwo ndipo anati, “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muone pamene palibe chitetezo.” |
Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.
Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.
idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m'dziko muno.
Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mzindawo ndi kuuzonda ndi kuupasula?
Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake.
Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.
Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeke pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo.
Pamenepo anyamata ozondawo analowa, natulutsa Rahabi, ndi atate wake ndi mai wake ndi abale ake, ndi onse anali nao; anatulutsanso achibale ake onse; nawaika kunja kwa chigono cha Israele.
Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m'mzinda, nanena naye, Utionetsetu polowera m'mzinda, ndipo tidzakuchitira chifundo.