Yoswa 2:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Tsono Yoswa, mwana wa Nuni, adatuma anthu aŵiri okazonda mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu, naŵalangiza kuti, “Pitani, mukalizonde dzikolo, makamaka mukazondenso mzinda wa Yeriko.” Motero adapita anthu ozondawo, nakafikira ku nyumba ya mkazi wina wadama dzina lake Rahabu. Kumeneko nkumene adagona. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Tsono Yoswa mwana wa Nuni anatuma anthu awiri okazonda dziko mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu. Iye anawawuza kuti, “Pitani mukaone dzikolo makamaka mzinda wa Yeriko.” Kotero iwo anapita ndipo anakafika ku nyumba ya mkazi wadama dzina lake Rahabe, ndipo anagona kumeneko. Onani mutuwo |