Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:34 - Buku Lopatulika

34 idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m'dziko muno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m'dziko muno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Ndipo mbale wanu wamng'onoyo mudzabwere naye kuno. Pamenepo ndiye ndidzadziŵe kuti sindinu azondi, koma ndinu okhulupirika. Mbale wanuyo ndidzambwezera kwa inu. Mukadzatero mungathe kumadzachitabe malonda m'dziko muno.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Koma mundibweretsere wotsirizayo kuti ndidziwedi kuti sindinu akazitape koma anthu achilungamo. Kenaka ndidzakubwezerani mʼbale wanuyu ndipo mukhoza kuchita malonda mʼdzikoli.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:34
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.


Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo.


Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao aakazi akhale aakazi athu, tiwapatse amenewa ana athu aakazi.


Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo wa Farao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.


koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho.


Osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabiya, ndi wa akazembe onse a madera.


chinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kumuka nayo kudziko la malonda, chinaiika m'mzinda wa amalonda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa