Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Atamasula matumba ao, aliyense adapeza kuti chikwama cha ndalama chinali momwe m'thumbamo. Ataona ndalamazo, iwowo pamodzi ndi bambo wao yemweyo adachita mantha kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Pamene amakhuthula matumba awo a tirigu aliyense anapeza kuti kathumba kake ka ndalama kali momwemo. Ataona zimenezi, iwo pamodzi ndi abambo awo anachita mantha kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:35
6 Mawu Ofanana  

nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala;


Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe.


ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.


Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.


watenga thumba la ndalama m'dzanja lake, tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa