Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 37:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono abale ake aja adachita naye kaduka kwambiri. Koma atate ake ankakhala akuziganiza zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Abale ake anamuchitira nsanje, koma abambo ake anasunga nkhaniyi mu mtima.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:11
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.


Ndipo abale ake ananka kukaweta zoweta za atate wao mu Sekemu.


Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko.


Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose ndi Aroni woyerayo wa Yehova.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndipo nsanje ya Efuremu idzachoka, ndi iwo amene avuta Yuda adzadulidwa; Efuremu sachitira nsanje Yuda, ndi Yuda sachitira nsanje Efuremu.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m'mtima mwanga.


Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.


Pakuti anazindikira kuti ansembe aakulu anampereka Iye mwanjiru.


Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake.


Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.


Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.


Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,


njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?


Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa