Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 37:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo iye anafotokozera atate wake ndi abale ake; ndipo atate wake anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo iye anafotokozera atate wake ndi abale ake; ndipo atate wake anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Maloto ameneŵa adauzanso bambo wake pamodzi ndi abale ake omwe aja. Atate ake adamdzudzula, adati, “Kodi maloto ameneŵa ngotani? Kodi ukuganiza kuti ine, mai wakoyu pamodzi ndi abale akoŵa, tidzakugwadira iwe?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Atawuza abambo ake ndi abale ake malotowa, abambo ake anamukalipira nati, “Ndi maloto anji umalotawa? Kodi uganiza kuti ine, amayi ako pamodzi ndi abale ako onsewa tingadzabwere kudzakugwandira iwe?”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:10
8 Mawu Ofanana  

Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.


pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.


Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.


Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.


Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.


Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa