Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 37:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono Yosefe adalotanso ena maloto, nauzanso abale akewo kuti, “Ndalotanso, ndipo ndaona dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zikundiŵeramira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Tsiku lina analotanso maloto ena, ndipo anafotokozera abale ake za malotowo. Iye anati, “Tamverani, ndinalotanso maloto ena. Ulendo uno dzuwa ndi mwezi pamodzi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zimandigwadira.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:9
19 Mawu Ofanana  

Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.


Ndipo iye anafotokozera atate wake ndi abale ake; ndipo atate wake anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi?


pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.


Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.


Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao.


Ndipo lotolo linabwerezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita.


Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.


Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.


Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.


Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake.


Mbuyanga anafunsa akapolo ake kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu?


Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe.


Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake.


Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao.


Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, ndi kuzipondereza.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa