Genesis 37:8 - Buku Lopatulika8 Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Apo abale akewo adamufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti udzakhala mfumu yathu? Kodi ndiye kuti iweyo nkudzatilamula ife?” Motero adadana naye koposa kale chifukwa cha malotowo ndi mau akewo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Abale ake aja anamufunsa nati, “Kodi ukuyesa kuti ungakhale mfumu yathu? Ungadzatilamuliredi iweyo?” Ndipo anamuda kuposa kale chifukwa cha maloto ake ndi zimene ankakonda kunena kwa abambo awo. Onani mutuwo |