2 Samueli 10:3 - Buku Lopatulika3 Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mzindawo ndi kuuzonda ndi kuupasula? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mudziwo ndi kuuzonda ndi kuupasula? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma akalonga a Aamoni adafunsa Hanuni mbuyawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide wakutumizirani anthu odzakupepesanimu, ndiye kuti akuchitira bambo wanu ulemu? Osati Davide watuma atumiki akewo kwa inu kuti adzafufuze ndi kuzonda mzindawu, ndipo kuti akauwona, auwononge?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni mbuye wawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi Davide sanawatumize anthuwa kuti adzaone mzinda wanu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” Onani mutuwo |