Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 10:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni mbuye wawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi Davide sanawatumize anthuwa kuti adzaone mzinda wanu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mzindawo ndi kuuzonda ndi kuupasula?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mudziwo ndi kuuzonda ndi kuupasula?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma akalonga a Aamoni adafunsa Hanuni mbuyawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide wakutumizirani anthu odzakupepesanimu, ndiye kuti akuchitira bambo wanu ulemu? Osati Davide watuma atumiki akewo kwa inu kuti adzafufuze ndi kuzonda mzindawu, ndipo kuti akauwona, auwononge?”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:3
6 Mawu Ofanana  

Tumizani mmodzi wa inu akamutenge mʼbale wanuyo ndipo ena nonsenu musungidwa mʼndende, kuti titsimikize ngati zimene mukunenazi ndi zoona. Apo ayi, pali Farao ndithu, inu ndinu akazitape!”


Pamenepo anakumbukira maloto aja amene analota za iwo ndipo anati, “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muone pamene palibe chitetezo.”


Inu mukumudziwa bwino Abineri mwana wa Neri. Iye anabwera kudzakunamizani ndi kudzaona mayendedwe anu ndiponso kudzaona zonse zimene mukuchita.”


atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?”


Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa.


Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa