Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 10:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anameta munthu aliyense mbali imodzi ya ndevu zake, ndi kudula zovala zake pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera, ndipo anawabweza kwawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Chomwecho Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndevu zao mbali imodzi, nadula zovala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chomwecho Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndevu zao mbali imodzi, nadula zovala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Choncho Hanuni adagwira atumiki a Davide aja, naŵameta ndevu mwachiperengedzu. Kenaka adaŵadulira zovala zao pakati mpaka m'chiwuno, naŵabweza kwao.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:4
8 Mawu Ofanana  

Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”


Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo, akupita ku malo awo achipembedzo kukalira; anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. Mutu uliwonse wametedwa mpala, ndipo ndevu zonse zametedwa.


momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto.


kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova.


“ ‘Musamamete mduliro kapena kumeta mʼmphepete mwa ndevu zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa