Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 41:1 - Buku Lopatulika

Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima panyanja.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Patapita zaka ziŵiri, Farao adaalota kuti waimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Patapita zaka ziwiri zathunthu, Farao analota atayimirira mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo,

Onani mutuwo



Genesis 41:1
21 Mawu Ofanana  

Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.


Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.


Ndipo Labani anati kwa iye, Eetu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi.


Ndipo anathawa iye ndi zonse anali nazo: ndipo anauka naoloka panyanja naloza nkhope yake iyang'anire kuphiri la Giliyadi.


Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukire Yosefe, koma anamuiwala.


Ndipo analota maloto onse awiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aejipito, amene anamangidwa m'kaidi.


Ndipo, taonani, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.


Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.


Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.


Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kumtsinje ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku mtsinjewo adzasanduka mwazi pamtunda.


Ndipo madzi adzaphwa m'mtsinje waukulu, ndipo mtsinje woyendamo madzi udzaphwa, nuuma.


nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aejipito, ng'ona yaikulu yakugona m'kati mwa mitsinje yake, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.


Ndi dziko la Ejipito lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine.


Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.


Pakuti dziko limene munkako kulilandira ndi losanga dziko la Ejipito lija mudatulukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;