Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Pamene Pilato anakhala pa mpando woweruza, mkazi wake anamutumizira uthenga uwu, “Musachite kanthu ndi munthuyo, ndi wosalakwa pakuti ndavutika kwambiri lero mʼmaloto chifukwa cha munthuyo.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:19
28 Mawu Ofanana  

Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.


Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.


Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe mu Ejipito,


Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya,


Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.


Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.


nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.


Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tilikulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachite kanthu kolakwa.


Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.


Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma mu Chihebri, Gabata.


Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.


Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,


Ndipo anawapirikitsa pa mpando wachiweruziro.


Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalire zimenezi.


Koma Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitire kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.


Potero, pamene adasonkhana pano, sindinachedwe, koma m'mawa mwake ndinakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.


Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikira ku Kesareya; ndipo m'mawa mwake anakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.


amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;


Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa