Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 4:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kumtsinje ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku mtsinjewo adzasanduka mwazi pamtunda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kunyanja ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma akakapanda kukhulupirira zizindikiro ziŵiri zonsezo, osafuna kumva zomwe ukaŵauzezo, ukatenge madzi a mu mtsinje wa Nailo, ukaŵathire pa nthaka youma. Madzi amenewo akasanduka magazi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 4:9
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.


Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mau a chizindikiro chotsirizachi.


Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'mtsinje ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.


Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa