Eksodo 4:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.” Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kumtsinje ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku mtsinjewo adzasanduka mwazi pamtunda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kunyanja ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Koma akakapanda kukhulupirira zizindikiro ziŵiri zonsezo, osafuna kumva zomwe ukaŵauzezo, ukatenge madzi a mu mtsinje wa Nailo, ukaŵathire pa nthaka youma. Madzi amenewo akasanduka magazi.” Onani mutuwo |