Eksodo 1:22 - Buku Lopatulika22 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amoyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Pamenepo Farao adalamula anthu ake kuti, “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa mwa Ahebri azimponya mu mtsinje wa Nailo, koma ana onse aakazi aziŵaleka, azikhala moyo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Pamenepo Farao analamulira anthu ake onse kuti, “Mwana wamwamuna aliyense akabadwa, mukamuponye mu mtsinje wa Nailo, koma wamkazi mulekeni akhale ndi moyo.” Onani mutuwo |