Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 1:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Pamenepo Farao analamulira anthu ake onse kuti, “Mwana wamwamuna aliyense akabadwa, mukamuponye mu mtsinje wa Nailo, koma wamkazi mulekeni akhale ndi moyo.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

22 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amoyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pamenepo Farao adalamula anthu ake kuti, “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa mwa Ahebri azimponya mu mtsinje wa Nailo, koma ana onse aakazi aziŵaleka, azikhala moyo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:22
11 Mawu Ofanana  

Patapita zaka ziwiri zathunthu, Farao analota atayimirira mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo,


amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake, kukonzera chiwembu atumiki ake.


“Mukamathandiza amayi a Chihebri pa mwala wochirira, muzionetsetsa kuti akabadwa mwana wamwamuna muzipha, koma akakhala wamkazi muzimuleka akhale ndi moyo.”


Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, “Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri.”


Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha, amathamangira kukhetsa magazi.


Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa. Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.


Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa; tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.


Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.


Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa