Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo, taonani, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo, taonani, zinatuluka m'nyanja ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nthaŵi yomweyo adangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zikutuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndipo anangoona ngʼombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zooneka bwino ndi zonenepa zikutuluka mu mtsinje muja ndi kuyamba kudya msipu wa mu mawango.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:2
6 Mawu Ofanana  

Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.


ndipo taona, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango;


Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'mtsinjemo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphepete mwa mtsinje.


Ngati gumbwa aphuka popanda chinyontho? Ngati manchedza amera popanda madzi?


Ndipo timitsinje tidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota.


Madambo oyandikana ndi mtsinje, pafupi ndi gombe la mtsinje, ndi zonse zobzala pamtsinje zidzauma, ndipo zidzachotsedwa, osakhalamo konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa