Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'mtsinjemo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphepete mwa mtsinje.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'nyanjamo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphete mwa nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kenaka mumtsinje momwemo mudatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi zofooka, zimene zidaima pa mtunda pafupi ndi ng'ombe zina zija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kenaka ngʼombe zina zazikazi zisanu ndi ziwiri zosaoneka bwino ndi zowonda zinatulukanso mu mtsinje wa Nailo ndipo zinayimirira pambali pa zina zija zimene zinali mʼmphepete mwa mtsinje uja.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:3
5 Mawu Ofanana  

ndipo taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinatuluka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Ejipito;


Ndipo, taonani, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.


Ndipo ng'ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka.


Mabondo anga agwedezeka chifukwa cha kusala; ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa