Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Genesis 22:1 - Buku Lopatulika Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee Ambuye.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!” Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” |
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.
Ndipo Isaki ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwanawankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?
Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta mu Sekemu? Tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda.
Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai.
Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.
Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;
Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isaki, ndipo iye mene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha;
Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe?
kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;
kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai.