ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.
Genesis 20:11 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti kuno kulibe ndi mmodzi yemwe woopa Mulungu, ndipo kuti akadandipha nkutenga mkazi wangayu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anayankha nati, “Ndinkaganiza kuti kuno kulibiretu munthu woopa Mulungu. Ndiye ndimati mwina adzandipha chifukwa cha mkazi wanga. |
ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.
Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.
Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.
ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.
Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;
Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.
Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.