Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita.
Genesis 19:9 - Buku Lopatulika Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iwowo adati, “Choka apa, wakudza iwe! Ndiwe yani iwe kuti ungatiwuze zoti tichite? Tachoka apa! Mwina mwake tingathe kukuzunza kwambiri kupambana iwowo.” Motero adamkankha Lotiyo, nasendera kuti akathyole chitseko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko. |
Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita.
Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'mizinda ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.
Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.
Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.
Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.
Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.
Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.
Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.
Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo.
Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.
Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.