Genesis 19:8 - Buku Lopatulika8 Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Taonanitu, ndili ndi ana akazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa chindwi langa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Onani, ine ndili ndi ana aakazi aŵiri, anamwali osadziŵa mwamuna. Bwanji ndikupatseni ana ameneŵa kuti muchite nawo zomwe mukufuna. Koma alendoŵa, musaŵachite kanthu kena kalikonse chifukwa ndi alendo anga, ndipo ndiyenera kuŵatchinjiriza.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Taonani, ine ndili ndi ana anga akazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Mundilole ndikutulutsireni amenewo ndipo muchite nawo zimene mungafune. Koma musachite chilichonse ndi anthuwa, pakuti iwowa ndi alendo anga ndipo ndiyenera kuwatchinjiriza.” Onani mutuwo |