Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 19:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono adaŵapempha kuti, “Inu abwenzi anga, musachite zimenezi chifukwa nkulakwa kwambiri kuchita zotere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 ndipo anati, “Ayi anzanga, musachite zinthu zoyipa zotere.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 19:7
13 Mawu Ofanana  

Koma asanagone, anthu a m'mzindamo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;


Ndipo Loti anatulukira kwa iwo pakhomo, natseka chambuyo pakhomo pake.


Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa.


Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.


Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.


ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;


Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;


Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana aakazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana aamuna a Israele.


Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.


Ndipo munthu mwini nyumba anawatulukira nanena nao, Iai, abale anga, musachite choipa chotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musachite chopusa ichi.


Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa