Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 10:13 - Buku Lopatulika

13 Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Chitsiru chimayamba ndi mau opusa, potsiriza zolankhula zake zimangokhala zamisala basi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa; potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 10:13
25 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?


Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa?


Nati iye, Andilange Mulungu naonjezeko, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati uti ukhale pa iye lero lino.


Yense wochenjera amachita mwanzeru; koma wopusa aonetsa utsiru.


Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.


Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake?


Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.


Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;


Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.


Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe.


Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.


Koma Afarisi ena anati, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika tsiku la Sabata?


Koma ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso;


Koma kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anati kwa mkazi wa Samisoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa