Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 7:6 - Buku Lopatulika

6 Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Musamapatsa agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zamtengowapatali, kuwopa kuti zingazipondereze, kenaka nkukutembenukirani ndi kukukadzulani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Musapatse agalu zinthu zopatulika; kapena musaponyere nkhumba ngale zanu. Pakuti ngati mutero, zidzaziponda ndipo pomwepo zidzakutembenukirani ndi kukudulani nthulinthuli.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 7:6
18 Mawu Ofanana  

Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.


Usalankhule m'makutu a wopusa; pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako.


Monga galu abweranso kumasanzi ake, momwemo chitsiru chichitanso zopusa zake.


Usayankhe chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti ungafanane nacho iwe wekha.


Ndipo Iye anayankha, nati, Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagalu.


Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.


Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.


paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;


Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula;


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.


Chidawachitikira iwo monga mwa mwambi woona uja, Galu wabwerera kumasanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m'thope.


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa