Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 2:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndipo munthuyo akanena kuti, “Apserezeretu mafutaŵa poyamba, pambuyo pake ndiye mutenge monga momwe mufunira,” mtumiki uja ankati, “Iyai, patsiretu tsopano pompano. Ngati sutero, ndichita kukulanda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ngati munthuyo anena kuti, “Apseretu mafuta poyamba, ndipo kenaka mutenge mmene mufunira,” mtumikiyo amayankha kuti, “Ayi ndipatse tsopano lino. Ngati sutero, ine nditenga molanda.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:16
9 Mawu Ofanana  

Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


Ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.


Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;


Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako.


Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.


Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa