Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.
Genesis 13:12 - Buku Lopatulika Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'mizinda ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'midzi ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abramu adakhala m'dziko la Kanani, koma Loti adakhazikika pakati pa mizinda yam'chigwa, nakamanga hema pafupi ndi mzinda wa Sodomu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. |
Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.
iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari).
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.
Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
ndipo anaononga mizindayo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m'mizindamo, ndi zimene zimera panthaka.
Ndipo panali pamene Mulungu anaononga mizinda ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga mizinda m'mene anakhalamo Loti.