Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 19:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo panali pamene Mulungu anaononga mizinda ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga mizinda m'mene anakhalamo Loti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo panali pamene Mulungu anaononga midzi ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga midzi m'mene anakhalamo Loti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Motero pamene Chauta ankaononga mizinda yam'chigwayo, adakumbukira pemphero la Abrahamu, ndipo adapulumutsa Loti ku chiwonongeko chimene chidasakaza mizinda ija m'mene Loti ankakhala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 19:29
21 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.


ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwake.


Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;


Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu, ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.


Popeza anakumbukira mau ake oyera, ndi Abrahamu mtumiki wake.


Akumbukira chipangano chake kosatha, mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;


Mundikumbukire, Yehova, monga momwe muvomerezana ndi anthu anu; mundionetsa chipulumutso chanu:


Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha.


Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.


Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.


chinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lachipululu.


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya ukapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.


Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo; musapenyerera kupulukira kwa anthu awa, kapena choipa chao, kapena tchimo lao;


Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.


ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa