Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 19:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo Loti anabwera kutuluka mu Zowari nakhala m'phiri ndi ana aakazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala mu Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake aakazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo Loti anabwera kutuluka m'Zowari nakhala m'phiri ndi ana akazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala m'Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake akazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Popeza kuti Loti ankaopa kukhala ku Zowari, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi aŵiri aja, adapita ku dziko lamapiri, onsewo nkumakakhala m'mapanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Loti ndi ana ake awiri aakazi anachoka ku Zowari nakakhala ku mapiri, chifukwa amachita mantha kukhala ku Zowari. Iye ndi ana ake awiri ankakhala mʼphanga.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 19:30
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.


Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi


Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.


taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;


Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.


Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.


Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.


ndi kumwera, ndi chidikha cha chigwa cha Yeriko, mzinda wa migwalangwa, kufikira ku Zowari.


munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha panjira zake zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa