Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 19:31 - Buku Lopatulika

31 Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe padziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita padziko lonse lapansi:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe pa dziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita pa dziko lonse lapansi:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Mwana wamkulu adauza mng'ono wake kuti, “Bambo athuŵa akukalamba tsopano, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe pa dziko lapansi woti angatikwatire, kuti tibale ana monga momwe zimachitikira zinthu pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Tsiku lina mwana wake wamkazi wamkulu anawuza mngʼono wake kuti, “Abambo athu ndi wokalamba ndipo palibe mwamuna aliyense pano woti atikwatire ndi kubereka ana monga mwa chikhalidwe cha pa dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 19:31
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.


Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake m'maso mwake.


ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.


Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.


Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.


Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.


Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu.


Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa