Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 19:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Angelo aŵiri aja adaloŵa m'Sodomumo madzulo ndi kachisisira, Loti atakhala pafupi ndi chipata cha mzindawo. Tsono Lotiyo atangoŵaona anthuwo, adaimirira nakaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, nati,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo ndipo Loti anali atakhala pansi pa chipata cha mzindawo. Loti atawaona, anayimirira ndi kukakumana nawo ndipo anaweramitsa mutu wake pansi mwaulemu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 19:1
15 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.


Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'mizinda ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.


Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.


Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova.


Koma anthu aja anatulutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo.


Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.


Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo.


Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi.


Muja ndinatuluka kunka kuchipata kumzinda, muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,


Mlendo sakagona pakhwalala, koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.


Okhala pachipata akamba za ine; ndipo oledzera andiimba.


Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba;


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa