Genesis 19:25 - Buku Lopatulika25 ndipo anaononga mizindayo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m'mizindamo, ndi zimene zimera panthaka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 ndipo anaononga midziyo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m'midzimo, ndi zimene zimera panthaka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Motero adaonongeratu mizinda imeneyi, pamodzi ndi chigwa chonse ndi anthu onse am'mizindamo, kuphatikizapo zomera zonse za m'dziko limenelo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Kotero, anawononga mizindayo, chigwa chonse pamodzi ndi onse okhala mʼmizindayo. Anawononganso zomera zonse za mʼdzikolo. Onani mutuwo |
Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.