Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 13:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Loti adadzisankhira chigwa chonse cha Yordani, napita kukakhala chakuvuma. Umu ndimo m'mene anthu aŵiriwo adasiyanirana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 13:11
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.


Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'mizinda ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.


Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo:


Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.


Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.


Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani, ndi iwo akusamalira malangizo anu.


Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.


Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.


Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.


osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.


Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa