ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira.
Genesis 10:19 - Buku Lopatulika Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mpaka ku malire a Kanani. Malirewo adayambira ku Sidoni namaloŵa ku Gerari mpaka ku Gaza ndi kumaloŵanso ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. |
ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira.
Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari).
Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu,
Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isaki ananka kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari.
Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri.
Iye watambasula dzanja lake panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira Kanani za amalonda, kupasula malinga ake.
Khala ndi manyazi, iwe Sidoni; chifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.
ndi anthu onse osakanizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi,
Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.
Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.
Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.
Kunena za Aavimu akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao).
Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.
nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira chochirira njala mu Israele, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena bulu.
gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko.