Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 13:18 - Buku Lopatulika

18 gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Gulu lina lidalunjika ku Betehoroni, ndipo lina lidalunjika ku malire oyang'anana ndi chigwa cha Zeboimu chakuchipululu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Gulu lina linalunjika ku Beti-Horoni, ndipo gulu lachitatu linalunjika ku malire oyangʼanana ndi chigwa cha Zeboimu cha ku chipululu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 13:18
12 Mawu Ofanana  

Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.


iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari).


ndi Yokomeamu ndi mabusa ake, ndi Betehoroni ndi mabusa ake,


Anamanganso Betehoroni wa kumtunda, ndi Betehoroni wa kunsi, mizinda ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;


Hadidi, Zeboimu, Nebalati,


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.


Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.


natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja.


Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum'mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda;


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa