Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 40:3 - Buku Lopatulika

Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nutchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nuchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Bokosi m'mene muli miyala yaumboni uliike m'menemo, ndipo bokosilo uliphimbe ndi nsalu kuti ulichinge.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani.

Onani mutuwo



Eksodo 40:3
16 Mawu Ofanana  

pakuti sindinakhale m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinakwera naye Israele, kufikira lero lino; koma ndakhala ndikuyenda m'mahema uku ndi uku.


Ndipo azipanga likasa la mtengo wakasiya: utali wake mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwake mkono ndi hafu, msinkhu wake mkono ndi hafu.


Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.


Ndipo uziomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi ntchito ya mmisiri;


chihema chokomanako, likasa la mboni, ndi chotetezerapo chili pamwamba pake, ndi zipangizo zonse za chihemacho;


likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka;


Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israele, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova analamula ndi kuti,


Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.


Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi chala chake pachotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi chala chake chakuno cha chotetezerapo kasanu ndi kawiri.


akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake aamuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,


Koma m'kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri;


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.