Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 31:6 - Buku Lopatulika

Ndipo Ine, taona, ndampatsa Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Ine, taona, ndampatsa Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndasankhanso Aholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani. Ndipo anthu ena onse aluso ndaŵapatsa nzeru zambiri zoti athe kupanga chinthu chilichonse chimene ndingakulamule kuti iwoŵa apange.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi:

Onani mutuwo



Eksodo 31:6
26 Mawu Ofanana  

taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.


Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kozokota mtengo, kuchita ntchito zilizonse.


Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova analamula;


Ndipo anaika m'mtima mwake kuti alangize ena, iye ndi Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani.


Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zilizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iliyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso.


Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israele, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova analamula ndi kuti,


Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga chihema ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri.


Ndi pamodzi naye Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.


Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao.


Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.