ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana aakazi a Dani, ndipo atate wake ndiye munthu wa ku Tiro, wodziwa kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira chopanga chilichonse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.