Eksodo 36:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga chihema ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Tsono amuna onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo, adapanga chihema cha Chauta ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Pa nsalu zonsezo adapetapo zithunzi za akerubi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi. Onani mutuwo |