Eksodo 28:12 - Buku Lopatulika Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uike miyala iŵiri imeneyi pa tizikwewo tam'mapewa ta efodi, ngati chikumbutso cha ana a Israele. Mwa njira imeneyi, Aroniyo azidzanyamula pa mapewa mainawo, ndipo Chauta azidzaŵakumbukira iwowo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. |
Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu.
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israele pa chapachifuwa cha chiweruzo pamtima pake, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale chikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
Nuike lubani loona ku mzere uliwonse, kuti likhale kumkate ngati chokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.
chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku chihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova.
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.
Za Benjamini anati, Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi Iye mokhazikika; am'phimba tsiku lonse, inde akhalitsa pakati pa mapewa ake.
Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.