Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 11:24 - Buku Lopatulika

24 ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 11:24
20 Mawu Ofanana  

Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake; Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.


Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.


Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.


Tiyeni, idyani chakudya changa; nimumwe vinyo wanga ndamsakaniza.


Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama.


Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.


Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.


Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.


Indetu ndinena kwa inu, kumene kulikonse Uthenga uwu Wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.


Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;


Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa.


Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa