Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:11 - Buku Lopatulika

11 Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Maina aowo uŵalembe mozokota pa miyala iŵiriyo, potsata luso la mmisiri wozokota miyala. Ndipo miyalayo uiike m'zoikamo zake zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:11
16 Mawu Ofanana  

Akadawazokota pathanthwe chikhalire, ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu!


maina asanu ndi limodzi pamwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pamwala unzake, mwa kubadwa kwao.


Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.


Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.


Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.


Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.


Ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golide maikidwe ake.


Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake.


Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele.


Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;


Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pamwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.


Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,


Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mau aakulu kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa