Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:10 - Buku Lopatulika

10 maina asanu ndi limodzi pamwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pamwala unzake, mwa kubadwa kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzake, mwa kubadwa kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pa mwala umodzi ulembepo maina asanu ndi limodzi, ndipo pa mwala winawo uchitenso chimodzimodzi. Ulembe mainawo motsatana malinga nkubadwa kwa ana a Israelewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:10
4 Mawu Ofanana  

Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.


Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.


Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulochepo maina a ana a Israele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa